Bungwe la Deposit Insurance Corporation (DIC) likudziwitsa anthu onse kuti nduna ya zachuma, Wolemekezeka a Simplex Chithyola Banda MP, pa 10 October 2024, adzakhazikitsa bungweli ku Bingu International Convention Centre ku Lilongwe. DIC ndi bungwe la boma lokhazikitsidwa ndi lamulo la Deposit Insurance Corporation Act, 2022 ndipo lidayamba kugwira ntchito pa 1 October 2023. Cholinga cha bungweli ndikuteteza ndalama zimene anthu amasungitsa ku mabanki, kuti  ngati banki itatsekedwa ndalamazo zikhale zotetezedwa. Kotero, kukhazikitsidwa kwa DIC kuthandizira kulimbitsa ntchito za mabungwe a zachuma m’dziko la Malawi komanso kulimbikitsa chikhulupiriro cha anthu pa mabanki.

Zina mwa ntchito za bungwe la DIC ndi:

  • Kuteteza ndalama zimene makasitomala amasungitsa m’mabanki ku Malawi kuno ndi cholinga cholimbikitsa chikhulupiriro pa ntchito za mabanki;
  • Kupereka thandizo la zachuma kumabanki munthawi ya mavuto, ndi cholinga chofuna kuti anthu asataye chikhulupiriro pa ntchito za mabanki;
  • Kubweza ndalama yosapitirira K1,000,000.00 kwa makasitomala a banki yomwe yatsekedwa, mogwirizana ndi lamulo;
  • Kuyang’anira mabanki amene akukumana ndi mavuto motsogozedwa ndi Mlembi wa Mabungwe a Zachuma wotchedwa Registrar of Financial Institutions;
  • Kusamalira ndi kugwiritsa ntchito  thumba la ndalama lothandizira makasitomala a banki yotsekedwa, mogwirizana ndi lamulo;
  • Kuunikira Mlembi wa Mabungwe a Zachuma ngati kuli kofunika kutseka banki imene ikugwa;
  • Kugwira ntchito yoyang’anira kapena kugulitsa katundu ndi kubweza ngongole za banki imene yatsekedwa motsogozedwa ndi Mlembi wa Mabungwe a Zachuma; ndi
  • Kukonza ndondomeko zoyendetsera ndi kuyang’anira thumba la ndalama lothandizira makasitomala a banki yotsekedwa.

Kuti mudziwe zambiri, lemberani:
The Director General
Deposit Insurance Corporation
P.O. Box 3118
BLANTYRE
Email: info@dic.mw